2 Akorinto 8:16-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.

17. Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala halo khama loposa, anaturukira kunka kwil inu mwini wace.

18. Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwace m'Uthenga Wabwino kuli m'Mipingo yonse;

19. ndipo si ici cokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'cisomo ici, cimene ticitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa cibvomerezo cathu;

20. ndi kupewa ici kuti wina angatichule za kucurukira kumene tikutumikira;

21. pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.

2 Akorinto 8