2 Akorinto 4:14-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. podziwa kuti iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu.

15. Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti cisomoco, cocurukitsidwa mwa unyinjiwo, cicurukitsire ciyamiko ku ulemerero wa Mulungu.

16. Cifukwa cace sitifoka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja ubvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku.

17. Pakuti cisautso cathu copepuka ca kanthawi citicitira ife kulemera koposa kwakukuru ndi kosatha kwa ulemerero;

18. popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka ziri za nthawi, koma zinthu zosaoneka ziri zosatha.

2 Akorinto 4