8. Pakuti sitikhoza kanthu pokana coonadi, koma pobvomereza coonadi.
9. Pakuti tikondwera, pamene ife tffoka ndi inu muli amphamvu; icinso tipempherera, ndicoungwiro wanu.
10. Cifukwa ca ici ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndiri pomwepo ndingacite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.
11. Cotsalira, abale, kondwerani, Mucitidwe angwiro; mutorithozedwe; khalani a mtima umodzi, khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa cikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.
12. Lankhulanani ndi cipsompsono copatulika.
13. Oyera mtima onse alankhula inu,
14. Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu, ndi cikondi ca Mulungu, ndi ciyanjano ca Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.