11. Cifukwa ninji? Cifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu.
12. Koma cimene ndicita, ndidzacitanso, kuti ndikawadulire cifukwa iwo akufuna cifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.
13. Pakuti otere ali atumwi onyenga, ocita ocenjerera, odzionetsa ngati atumwi a Kristu,
14. Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.
15. Cifukwa cace sikuli kanthu kwakukuru ngatinso atumiki ace adzionetsa monga atumiki a cilungamo; amene cimariziro cao cidzakhala monga nchito zao.
16. Ndinenanso, Munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang'ono.