3. Pakuti pakuyendayenda m'thupi, siticita nkhondo monga mwa thupi,
4. (pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);
5. ndi kugwetsa matsutsano, ndi cokwezeka conse cimene cidzikweza pokana ddziwitso ca Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu;