2 Akorinto 10:3-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Pakuti pakuyendayenda m'thupi, siticita nkhondo monga mwa thupi,

4. (pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);

5. ndi kugwetsa matsutsano, ndi cokwezeka conse cimene cidzikweza pokana ddziwitso ca Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu;

6. ndi kukhala okonzeka Irubwezera cilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa.

7. Kodi mupenyera zopenyeka pamaso? Ngati wina alimbika mwa yekha kuti ali wa Kristu, ayesere icinso mwa iye yekha, kuti monga iye ali wa Kristu, koteronso ife.

8. Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kocurukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye ku kumangirira, ndipo si ku kugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;

9. kuti ndisaoneke monga ngati kukuopsani mwa akalatawo.

10. Pakuti, akalatatu, ati, ndiwo olemera, ndi amphamvu; koma maonekedwe a thupi lace ngofoka, ndi mau ace ngacabe.

2 Akorinto 10