6. Koma ngati tisautsidwa, kuli cifukwa ca citonthozo ndi cipulumutso canu; ngati titonthozedwa, kuli kwa citonthozo canu cimene cicititsa mwa kupirira kwa masautso omwewo amene ifenso timva.
7. Ndipo ciyembekezo cathu ca kwa inu ncokbazikika; podziwa kuti monga muli oyanjana ndi masautsowo, koteronso ndi citonthozo.
8. Pakuti sitifuna abale, kuti mukhale osadziwa za cisautso cathu tinakomana naco m'Asiya, kuti tinathodwa kwakukuru, koposa mphamvu yathu, kotero kuti tinada nkhawa ngakhale za moyo wathu;