1 Yohane 5:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Umo tizindikira kuti tikonda ana a Mulungu, pamene tikonda Mulungu, ndi kucita malamulo ace.

3. Pakuti ici ndi cikondi ca Mulungu, kuti tisunge malamulo ace: ndipo malamulo ace sali olemetsa.

4. Pakuti ciri conse cabadwa mwa Mulungu cililaka dziko lapansi; ndipo ici ndi cilako tililaka naco dziko lapansi, ndico cikhulupiriro cathu.

5. Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu

6. iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi; ndiye Yesu Kristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi.

7. Ndipo Mzimu ndiye wakucita umboni, cifukwa Mzimu ndiye coonadi,

8. Pakuti pali atatu akucita umboni, Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.

1 Yohane 5