16. Pakuti ciri conse ca m'dziko lapansi, cilakolakoca thupi ndi cilakolako ca maso, matamandidwe a moyo, sizicokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.
17. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi cilakolako cace; koma iye amene acita cifuniro ca Mulungu akhala ku nthawi yonse.
18. Ana inu, ndi nthawi yorsirtza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana. Krisru akudza, ngakhale tsopano alipo okana Kristu ambiri; mwa ici tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.
19. Anaturuka mwa ife, komatu sanali a ife; pakuti akadakhala a ife akadakhalabe ndi ife, koma kudatero 1 kuti aonekere kutr sali onse a ife.