4. ndipo izi tilemba ife, kuti cimwemwe cathu cikwaniridwe.
5. Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa iye monse mulibe mdima.
6. Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo siticita coonadi;
7. koma ngati tiyenda m'kuunika, mongalye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzace, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wace utisambitsa kuticotsera ucimo wonse.
8. Tikati kuti tiribe ucimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe coonadi.