1. Onse amene ali akapolo a m'goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi ciphunzitso zisacitidwe mwano.
2. Ndipo iwo akukhala nao ambuye okhulupira, asawapeputse popeza ali abale; koma makamaka awatumikire popeza ali okhulupira ndi okondedwa, oyanjana nao pa cokomaco, Izi uphunzitse, nucenjeze.
3. Ngati munthu aphunzitsa zina, wosabvomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Kristu, ndi ciphunzitsoco ciri monga mwa cipembedzo:
4. iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayarukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zieokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;
5. makani opanda pace a anthu oipsika nzeru ndi ocotseka coonadi, akuyesa kuti cipembedzo cipindulitsa.