10. wa mbiri ya nchito zabwino; ngati walera ana, ngati wacereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a nzera mtima, ngati wathapdiza osautsidwa, ngati anatsatadi nchito zonse zabwino.
11. Koma amasiyeang'ono uwakane; pakuti pamene ayambakumcitira Kristu cipongwe afuna kukwatiwa;
12. pokhala naco citsutso, popeza adataya cikhulupiriro cao coyamba.
13. Ndipo aphunziraponso kucita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pace, nacita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.
14. Cifukwa cace nditi akwatiwe amasiye ang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa cifukwa kwa mdaniyo cakulalatira;
15. pakuti adayamba enakupatuka ndi kutsata Satana.
16. Ngati mkazi wina wokhulupira ali nao amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingowo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.
17. Akuru akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akucititsa m'mau ndi m'ciphunzitso.