5. Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu?
6. Asakhale wophunza, kuti podzitukumula ungamgwere mlandu wa mdierekezi.
7. Kuyeneranso kuti iwo akunja adzakhoza kumcitira umboni wabwino; kuti ungamgwere mtonzo, ndi msampha wa mdierekezi.
8. Momwemonso atumiki akhale olemekezeka, osanena pawiri, osamwetsa vinyo, osati a cisiriro conyansa;
9. okhala naco cinsinsi ca cikhulupiriro m'cikumbu mtima coona.
10. Koma iwonso ayambe ayesedwe; pamenepo atumikire, akakhala opanda cifukwa.
11. Momwemonso akazi akhale olemekezeka, osadierekeza, odzisunga, okhulupirika m'zonse.
12. Atumiki akhale mwamuna wa mkazi mmodzi, akuweruza bwino ana ao, ndi iwo a m'nyumba yao ya iwo okha.