15. kuti udziwe kuyenedwa kwace pokhala m'nyumba ya Mulungu, ndiye Eklesia wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mcirikizo wa coonadi.
16. Ndipo pobvomerezeka, cinsinsi ca kucitira Mulungu ulemu ncacikuru: iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa m'ulemerero.