1. Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna nchito yabwino.
2. Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kucereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;
3. wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba cuma;
4. woweruza bwino nyumba yace ya iye yekha, wakukhala nao ana ace omvera iye ndi kulemekezeka konse.