1 Timoteo 3:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mauwa ali okhulupirika, ngati munthu akhumba udindo wa woyang'anira, aifuna nchito yabwino.

2. Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kucereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

3. wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba cuma;

1 Timoteo 3