1 Timoteo 2:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale cete.

13. Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva;

14. ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa;

15. koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'cikhulupiriro ndi cikondi ndi ciyeretso pamodzi ndi cidziletso.

1 Timoteo 2