8. ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaretapo; nimuike zokometsera zagolidi, zimene muzipereka kwa iye ngati nsembe yoparamula, m'bokosi pam bali pace; nimulitumize licoke.
9. Ndipo muyang'anire, ngati likwera pa njira ya malire ace ace ku Betisemesi, iye anaticitira coipa ici cacikuru; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, siliri lace; langotigwera tsokali.
10. Ndipo anthuwo anatero; natenga ng'ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagareta, natsekera anao kwao;
11. naika likasa la Yehova pagaretapo, ndi bokosi m'mene munali mbewa zagolidi ndi zifanizo za mafundo ao.
12. Ndipo ng'ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betisemesi, niziyenda mumseu, zirikulira poyenda; sizinapambukira ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betisemesi.