9. Ndipo kunali atafika nalo, dzanja la Yehova linatsutsa mudziwo ndi kusautsa kwakukuru; ndipo anazunza anthu a mudziwo, akuru ndi ang'ono; ndi mafundo anawabuka.
10. Cifukwa cace anatumiza likasa la Mulungu ku Ekroni. Ndipo kunali pofika likasalo ku Ekroni, a ku Ekroni anapfuula nati, Anadzatitulira likasa la Mulungu wa Israyeli, kutipha ife ndi ana athu.
11. Cifukwa cace anatumiza, nasonkhanitsa mafumu onse a Afilisti, ndipo iwowa anati, Cotsani likasa la Mulungu wa Israyeli, lipitenso kumalo kwace, kuti lingationonge ife, ndi anthu athu; pakuti kunali kusautsa koopsa m'mudzi monse; dzanja la Mulungu linabvutadi pamenepo.
12. Ndipo amene anapanda kufa anagwidwa ndi mafundowo; ndi kulira kwa mudziwo kunakwera kumwamba.