8. Ndipo kunali m'mawa mwace, pakubwera Afilisti kubvula akufawo, anapeza Sauli ndi ana ace atatu ali akufa m'phiri la Giliboa.
9. Ndipo anadula mutu wace, natenga zida zace, natumiza m'dziko lonse la Afilisti mithenga yolalikira ku nyumba ya milungu yao, ndi kwa anthu.
10. Ndipo anaika zida zace m'nyumba ya Asitarote; napacika mtembo wace ku linga la ku Betisani.
11. Koma pamene a ku Jabezi Gileadi anamva zimene Afilisti anamcitira Sauli,
12. ngwazi zonse zinanyamuka ndi kucezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Sauli, ndi mitembo ya ana ace, pa linga la Betisani; nafika ku Jabezi Gileadi naitentha kumeneko.
13. Natenga mafupa ao nawaika patsinde pa mtengo uli m'Jabezi, nasala kudya masiku asanu ndi awiri.