9. Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa cimene anacita Sauli, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; cifukwa ninji tsono mulikuchera moyo wanga msampha, kundifetsa.
10. Ndipo Sauli anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe cilango cidzakugwera cifukwa ca cinthu ici.
11. Pomwepo mkaziyo anati, Ndikuukitsireni yani? Nati iye, Undiukitsire Samueli.
12. Ndipo mkaziyo pakuona Samueli, anapfuula ndi mau akuru; ndi mkaziyo analankhula ndi Sauli, nati, Munandinyengeranji? popeza inu ndinu Sauli.
13. Ndipo mfumuvo inanena naye, Usaope, kodi ulikuona ciani? Mkaziyo nanena ndi Sauli, Ndirikuona milungu irikukwera kuturuka m'kati mwa dziko.