1 Petro 4:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. koposa zonse mukhale naco cikondano ceni ceni mwa inu nokha; pakuti cikondano cikwiriritsa unyinji wa macimo;

9. mucerezane wina ndi mnzace, osadandaula:

10. monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a cisomo ca mitundu mitundu ca Mulungu;

11. akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, acite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Kristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu ku nthawi za nthawi. Amen.

12. Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale cakukuyesani, ngati cinthu cacilendo cacitika nanu:

13. koma popeza mulawana ndi Kristu zowawa zace, kondwerani; kutinso pa bvumbulutso la ulemerero wace mukakondwere kwakukurukuru.

14. Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.

15. Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wocita zoipa, kapena ngati wodudukira;

16. koma akamva zowawa ngati Mkristu asacite manyazi; koma alemekeze Mulungu m'dzina ili.

17. Cifukwa yafika nthawi kuti ciweruziro ciyambe pa nyumba ya Mulungu; komangati ciyamba ndi ife, citsiriziro ca iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu cidzakhala ciani?

1 Petro 4