1 Petro 4:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Popeza Kristu adamva zowawa m'thupi, mudzikonzere mtima womwewo; pakuti iye amene adamva zowawa m'thupi walekana nalo cimo;

2. kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsata zilakolako za anthu, koma cifuniro ca Mulungu.

3. Pakuti nthawi yapitayi idatifikira kucita cifuno ca amitundu, poyendayenda ife m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;

4. m'menemo ayesa ncacilendo kuti simuthamanga nao kufikira kusefukira komwe kwa citayiko, nakucitirani mwano;

1 Petro 4