1 Petro 3:8-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Cotsalira, khalani nonse a mdma umodzi, ocitirana cifundo, okondana ndi abale, acisoni, odzicepetsa:

9. osabwezera coipa ndi coipa, kapena cipongwe ndi cipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ici mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.

10. Pakuti,iye wofuna kukonda moyo,Ndi kuona masiku abwino,Aletse lilime lace lisanene coipa,Ndi milomo yace isalankhule cinyengo;

11. j Ndipo apatuke pacoipa, nacite cabwino;Afunefune mtendere ndi kuulondola.

12. Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama,Ndi makutu ace akumva rembedzo lao;Koma nkhope ya Ambuye iri pa ocita zoipa,

1 Petro 3