1 Petro 2:9-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe acifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mw ni wace, kotero kuti mukalakire zoposazo za iye amene anakuitanani muturuke mumdima, mulowe kuunika kwace kodabwitsa;

10. inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandira cifundo, koma tsopano mwalandira cifundo.

11. Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zicita nkhondo pa moyo;

12. ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ocita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona nchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.

1 Petro 2