1 Petro 2:23-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. 4 amene pocitidwa cipongwe sanabwezera cipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa, koma 5 anapereka mlandu kwa iye woweruza kolungama;

24. 6 amene anasenza macimo athu mwini yekha m'thupi mwace pamtanda, kuti ife, 7 titafa kumacimo, tikakhale ndi moyo kutsata cilungamo; 8 ameneyo mikwingwirima yace munaciritsidwa nayo.

25. Pakuti 9 munalikusocera ngati nkhosa; koma rsopano mwabwera kwa 10 Mbusa ndi Woyang'anira wa moyo wanu.

1 Petro 2