1 Petro 1:17-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo mukamuitana ngati Alate, iye amene aweruza monga mwa nchito ya yense, wopanda tsankhu, khalani ndi mantha nthawi ya cilendo canu;

18. podziwa kuti simunaomboledwa ndi zobvunda, golidi ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu acabe ocokera kwa makolo anu:

19. koma 1 ndi mwazi wa mtengo wace wapatali 2 monga wa mwana wa nkhosa wopanda cirema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu:

20. 3 amene anazindikirikatu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa citsiriziro ca nthawi,

21. cifukwa ca inu amene mwa rye mukhulupirira Mulungu 4 wakwnuukitsa iye kwa akufa, ndi kumpatsa iye ulemerero; kotero kuti cikhulupiriro canu ndi ciyembekezo canu cikhale pa Mulungu.

22. Popeza 5 mwayeretsa moyo wanu pakumvera coonadi kuti 6 mukakonde abale ndi cikondi cosanyenga, mukondane kweni kweni kucokera kumtima;

23. 7 inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.

24. Popeza,8 Anthu onse akunga udzu,Ndi ulemerero waowonse ngad duwa la udzu.Udzuwo ungotota, ndi duwa lace lingogwa;

25. 9 Koma Mau a Mulungu akhala cikhalire.Ndipo 10 mau olalikidwa kwa Inu ndi jawo.

1 Petro 1