1. Ndipo Benjamini anabala Bela mwana wace vyoyamba, Asibeli waciwiri, ndi Ahara wacitatu,
2. Noha wacinai, ndi Rafa wacisanu.
3. Ndi Bela anali ndi ana: Adara, ndi Gera, ndi Abihudi,
4. ndi Abisuwa, ndi Namani, ndi Ahowa,
5. ndi Gera, ndi Sefufani, ndi Huramu.
6. Ndi ana a Ehudi ndi awa: ndiwo akuru a nyumba za makolo ao a iwo okhala ku Geba, ndipo anawatenga ndende kumka ku Manahati,
7. natenga ndende Namani, ndi Ahiya, ndi Gera, ndipo, anabala Uza, ndi Ahihudi.