1 Mbiri 7:36-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ana a Zofa: Suwa, ndi Harineferi, ndi Sauli, ndi Beri, ndi Imra,

37. Bezeri, ndi Hndi, ndi Sama, ndi Silisa, ndi Itirani, ndi Beera.

38. Ndi ana a Yeteri: Yefune, ndi Pisipa, ndi Ara.

39. Ndi ana a Ula: Ara, ndi Hanieli, ndi Rizya.

40. Awa onse ndiwo ana a Aseri, akuru a nyumba za makolo ao, ngwazi zosankhika ndi zamphamvu, akuru mwa akalonga. Oyesedwa mwa cibadwidwe cao otumikira kunkhondo ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi.

1 Mbiri 7