12. Sufimu yemwe ndi Hupimu ana a Iri, ndi Husimu mwana wa Aheri.
13. Ana a Nafuali: Yazieli, ndi Guni, ndi Yezeri, ndi Salumu, ana a Bila.
14. Ana a Manase ndiwo Asrieli amene mkazi wace anambala, Koma mkazi wace wamng'ono Maramu anabala Makiri atate wa Gileadi;
15. ndi Makiri anadzitengera mkazi, mlongo wace wa Hupimu ndi Supimu, dzina lace ndiye Maaka. Ndipo dzina la mwana waciwiri wa Manase ndiye Tselofekadi. Ndi Tselofekadi anali ndi ana akazi.