28. Ndi ana a Samueli: woyamba Yoeli, ndi waciwiri Abiya.
29. Ana a Merari: Mali, Libni mwana wace, Simei mwana wace, Uza mwana wace,
30. Simeya mwana wace, Hagiya mwana wace, Asaya mwana wace.
31. Ndipo iwo aja Davide anawaimika a udindo wa nyimbo m'nyumba ya Yehova, litafikira kupumula likasalo, ndi awa.