1. Ana a Levi: Gerisomu, Kohati, ndi Merari.
2. Ndi ana a Kohati: Amramu, Izara, ndi Hebroni, ndi Uzieli.
3. Ndi ana a Amramu: Aroni, ndi Mose, ndi Miriamu. Ndi ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
4. Eleazara anabala Pinehasi, Pinehasi anabala Abisua,
5. ndi Abisua anabala Buki, ndi Buki anabala Uzi,
6. ndi Uzi anabala Zerahiya, ndi Zerahiya anabala Merayoti,
7. Merayoti anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubu,
8. ndi Ahitubu anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Ahimaazi,
9. ndi Ahimaazi anabala Azariya, ndi Azariya anabala Yohanani,
10. ndi Yohanani anabala Azariya (ndiye amene anacita nchito ya nsembe m'nyumba anaimanga Solomo m'Yerusalemu),
11. ndi Azariya anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubu,
12. ndi Ahitubu anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Salumu,
13. ndi Salumu anabala Hilikiya, ndi Hilikiya anabala Azariya,
14. ndi Azariya anabala Seraya, ndi Seraya anabala Yehozadaki,
15. ndi Yehozadaki analowa undende muja Yehova anatenga ndende Yuda ndi Yerusalemu ndi dzanja la Nebukadinezara.
16. Ana a Levi: Gerisomu, Kohati ndi Merari.