1 Mbiri 5:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndi abale ace monga mwa mabanja ao, powerenga cibadwidwe ca mibadwo yao: akuru ndiwo Yeyeli, ndi Zekariya,

8. ndi Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yoeli, wokhala ku Aroeri, ndi kufikira ku Nebo ndi Baala-meoni;

9. ndi kum'mawa anakhala mpaka polowera kucipululu kuyambira mtsinje wa Firate; pakuti zoweta zao zinacuruka m'dziko la Gileadi.

10. Ndipo masiku a Sauli anagwirana nkhondo ndi Ahagiri, amene adagwa ndi dzanja lao; ndipo anakhala m'mahema mwao kum'mawa konse kwa Gileadi.

11. Ndi ana a Gadi anakhala pandunji pao m'dziko la Basana mpaka Saleka:

12. Yoeli mkuru wao, ndi Safamu waciwiri, ndi Yanai, ndi Safati m'Basana;

1 Mbiri 5