1 Mbiri 4:5-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo Asuri atate wa Tekowa anali nao akazi awiri: Hela, ndi Naara.

6. Ndi Naara anambalira Ahuzamu, ndi Heferi, ndi Temeni, ndi Hahastario Iwo ndiwo ana a Naara.

7. Ndi ana a Hela ndiwo Zereti, lzara, ndi Etinani.

8. Ndipo Hakozi anabala Anubu, ndi Zobeba, ndi mabanja a Ahareli mwana wa Harumu.

1 Mbiri 4