16. Ndi ana a Yehoyakimu: Yekoniya mwana wace, Zedekiya mwana wace.
17. Ndi mwana wa Yekoniya: Asiri, Sealitiyeli mwana wace,
18. ndi Malikiramu, ndi Pedaya, ndi Senazara, Yekamiya, Hosama, Nedabiya.
19. Ndi ana a Pedaya: Zerubabeli, ndi Simei; ndi ana a Zerubabeli: Mesulamu, ndi Hananiya; ndipo Selomiti ndiye mlongo wao,
20. ndi Hasuba, ndi Oheli, ndi Berekiya, ndi Hasadiya, ndi Yusabi-hesedi; asanu.
21. Ndi ana a Hananiya: Pelatiya, ndi Yesaya, ana a Refaya, ana a Arinani, ana a Obadiya, ana a Sekaniya.