4. Komatu Yehova Mulungu wa Israyeli anasankha ine m'nyumba yonse ya atate wanga, ndikhale mfumu ya Israyeli kosatha; pakuti anasankhiratu Yuda akhale mtsogoleri, ndi m'nyumba ya Yuda nyumba ya atate wanga, ndi mwa ana a atate wanga ndinamkomera ndine, andilonge ufumu wa Israyeli yense;
5. ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana amuna ambiri), anasankha Solomo mwana wanga akhale pa mpando wacifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israyeli.
6. Ndipo anati kwa ine, Solomo mwana wako ndiye adzandimangira nyumba yanga ndi mabwalo anga; pakuti ndamsankha akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala atate wace.
7. Ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wace kosatha, akalimbika kucita malamulo anga ndi maweruzo anga monga lero lino.
8. Ndipo tsopano, pamaso pa Aisrayeli onse, khamu la Yehova, ndi m'makutu a Mulungu wathu, sungani, nimufunefune malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti mukhale nalo lanu lanu dziko lokoma ili, ndi kulisiyira ana anu pambuyo panu colowa cao kosalekeza.
9. Ndipo iwe Solomo mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna iye udzampeza, koma ukamsiya iye adzakusiya kosatha.