7. Ndipo ciwerengo cao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa ayimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu.
8. Ndipo anacita maere pa udikiro wao, analingana onse, ang'ono ndi akuru, mphunzitsi ndi wophunzira.
9. Maere oyamba tsono anagwera a banja la Asafu ndiye Yosefe; waciwiri Gedaliya, iye ndi abale ace, ndi ana ace khumi ndi awiri;
10. wacitatu Zakuri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
11. wacinai Izri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
12. wacisanu Netaniya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
13. wacisanu ndi cimodzi Bukiya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
14. wacisanu ndi ciwiri Yesarela: ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
15. wacisanu ndi citatu Yesaya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
16. wacisanu ndi cinai Mataniya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri:
17. wakhumi Simeyi, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
18. wakhumi ndi cimodzi Azareli, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;