1. Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi ciwerengo ca anchito monga mwa kutumikira kwao ndko:
2. a ana a Asafu: Zakuri, ndi Yosefe, ndi Netaniya, ndi Asarela, ana a Asafu; mwa cilangizo ca Asafu, wakunenera mwa cilangizo ca mfumu.