3. Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleke wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao m'utumiki wao.
4. Ndipo anapeza kuti amuna akuru a ana a Eleazara anacuruka, a ana a Itamara anacepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akuru a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu.
5. Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe.
6. Ndi Semaya mwana wa Netaneli mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleke mwana wa Abyatara, a akuru a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lace ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.
7. Ndipo maere oyamba anamgwera Yehoyaribu, waciwiri Yedaya,