18. wa makumi awiri ndi citatu Delaya, wa makumi awiri ndi cinai Miziya.
19. Awa ndi malongosoledwe ao m'utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa ciweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israyeli anamlamulira.
20. Ndipo wa ana otsala a Levi: wa ana a Amiramu, Subaeli; wa ana a Subaeli, Yedeya.
21. Wa Rehabiya: wa ana a Rehabiya, mkuru ndi Isiya.
22. Wa Aizari: Selomoti; wa ana a Selomoti, Yahati.