1 Mbiri 24:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.

2. Koma Nadabu ndi Abihu anafa, atate wao akali ndi moyo, opanda ana; momwemo Eleazara ndi ltamara anacita nchito ya nsembe.

3. Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleke wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao m'utumiki wao.

4. Ndipo anapeza kuti amuna akuru a ana a Eleazara anacuruka, a ana a Itamara anacepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akuru a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu.

5. Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe.

6. Ndi Semaya mwana wa Netaneli mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleke mwana wa Abyatara, a akuru a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lace ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.

1 Mbiri 24