1 Mbiri 2:48-51 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

48. Maka mkazi wamng'ono wa Kalebi anabala Seberi, ndi Tirana.

49. Iyeyu anabalanso Safa atate wa Madimana, Seva atate wa Makibena, ndi atate wa Gibeya; ndi mwana wamkazi wa Kalebi ndiye Akisa.

50. Ana a Kalebi ndi awa: mwana wa Huri, mwana woyamba wa Efrata, Sobali atate wa Kiriate Yearimu.

51. Salma atate wa Betelehemu, Harefi atate wa Betigaderi.

1 Mbiri 2