41. ndi Salumu anabala Yekamiya, ndi Yekamiya anabala Elisama.
42. Ndi ana a Kalebi mbale wa Yerameli ndiwo Mesa mwana wace woyamba, ndiye atate wa Zifi; ndi ana a Maresa atate wa Hebroni.
43. Ndi ana a Hebroni: Kora, ndi Tapuwa, ndi Rekemu, ndi Sema.
44. Ndi Sema anabala Rahamu atate wa Yorikeamu, ndi Rekemu anabala Samai.
45. Ndi mwana wa Samai ndiye Maoni; ndipo Maoni ndiye atate wa Betizuri.
46. Ndi Efa mkazi wamng'ono wa Kalebi anabala Harani, ndi Moza, ndi Gazezi; ndi Harani anabala Gazezi.
47. Ndi ana a Yadai: Regemu, ndi Yotamu, ndi Gesam, ndi Peleti, ndi Efa, ndi Safa.
48. Maka mkazi wamng'ono wa Kalebi anabala Seberi, ndi Tirana.