4. Ndi Tamari mpongozi wace anambalira Perezi ndi Zera. Ana amuna onse a Yuda ndiwo asanu.
5. Ana a Perezi: Hezironi, ndi Hamuli.
6. Ndi ana a Zera: Zimri, ndi Etani, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Dara; onse pamodzi ndi asanu.
7. Ndi ana a Karmi: Akari wobvuta Israyeliyo, amene analakwira coperekedwa ciperekereco.
8. Ndi mwana wa Etani: Azariya.
9. Ndi ana a Hezironi anambadwirawo: Yerameli, ndi Ramu, ndi Kelubai.
10. Ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni kalonga wa ana a Yuda;
11. ndi Nasoni anabala Salima, ndi Salima anabala Boazi,
12. ndi Boazi anabala Obedi, ndi Obedi anabala Jese,