1 Mbiri 2:27-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Ndipo ana a Ramu mwana woyamba wa Yerameli ndiwo Maazi, ndi Yamini, ndi Ekeri.

28. Ndi ana a Onamu ndiwo Samai, ndi Yada; ndi ana a Samai: Nadabu, ndi Abisuri.

29. Ndipo dzina la mkazi wa Abisuri ndiye Abihaili; ndipo anambalira Abani, ndi Molidi.

30. Ndi ana a Nadabu: Seledi ndi Apaimu; koma Seledi anamwalira wopanda ana.

31. Ndi mwana wa Apaimu: lsi. Ndi mwana wa lsi: Sesani. Ndi mwana wa Sesani: Alai.

32. Ndi ana a Yada mbale wa Samai: Yeteri, ndi Yonatani; namwalira: Yeteri wopanda ana.

33. Ndi ana a, Yonatani: Peleti, ndi Zaza. Ndiwo ana a Yerameli.

34. Ndipo Sesani analibe ana amuna, koma ana akazi. Ndi Sesani anali naye mnyamata M-aigupto dzina lace ndiye Yara.

35. Ndipo Sesani anampatsa Yara mnyamata wace mwana wace wamkazi akhale mkazi wace, ndipo anambalira Atai.

36. Ndipo Atai anabala Natani, ndi Natani anabala Zabadi,

37. ndi Zabadi anabala Efilali, ndi Efilali anabala Obedi,

38. ndi Obedi anabala Yehu, ndi Yehu anabala Azariya,

39. ndi Azariya anabala Helezi, ndi Helezi anabala Eleasa,

40. ndi Eleasa anabala Sismai, ndi Sismai anabala Salumu,

41. ndi Salumu anabala Yekamiya, ndi Yekamiya anabala Elisama.

42. Ndi ana a Kalebi mbale wa Yerameli ndiwo Mesa mwana wace woyamba, ndiye atate wa Zifi; ndi ana a Maresa atate wa Hebroni.

1 Mbiri 2