26. Ndipo Yerameli anali naye mkazi wina dzina lace ndiye Atara, ndiye mace wa Onamu.
27. Ndipo ana a Ramu mwana woyamba wa Yerameli ndiwo Maazi, ndi Yamini, ndi Ekeri.
28. Ndi ana a Onamu ndiwo Samai, ndi Yada; ndi ana a Samai: Nadabu, ndi Abisuri.
29. Ndipo dzina la mkazi wa Abisuri ndiye Abihaili; ndipo anambalira Abani, ndi Molidi.
30. Ndi ana a Nadabu: Seledi ndi Apaimu; koma Seledi anamwalira wopanda ana.
31. Ndi mwana wa Apaimu: lsi. Ndi mwana wa lsi: Sesani. Ndi mwana wa Sesani: Alai.
32. Ndi ana a Yada mbale wa Samai: Yeteri, ndi Yonatani; namwalira: Yeteri wopanda ana.
33. Ndi ana a, Yonatani: Peleti, ndi Zaza. Ndiwo ana a Yerameli.
34. Ndipo Sesani analibe ana amuna, koma ana akazi. Ndi Sesani anali naye mnyamata M-aigupto dzina lace ndiye Yara.
35. Ndipo Sesani anampatsa Yara mnyamata wace mwana wace wamkazi akhale mkazi wace, ndipo anambalira Atai.
36. Ndipo Atai anabala Natani, ndi Natani anabala Zabadi,