1 Mbiri 2:24-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo atafa Hezroni m'Kalebi-Efrata, Abiya mkazi wa Hezroni anambalira Asini atate wa Tekoa.

25. Ndi ana a Yerameli mwana woyamba wa Hezroni ndiwo: woyamba Ramu, ndi Buna, ndi Oreni, ndi Ozemu, ndi Ahiya.

26. Ndipo Yerameli anali naye mkazi wina dzina lace ndiye Atara, ndiye mace wa Onamu.

27. Ndipo ana a Ramu mwana woyamba wa Yerameli ndiwo Maazi, ndi Yamini, ndi Ekeri.

28. Ndi ana a Onamu ndiwo Samai, ndi Yada; ndi ana a Samai: Nadabu, ndi Abisuri.

29. Ndipo dzina la mkazi wa Abisuri ndiye Abihaili; ndipo anambalira Abani, ndi Molidi.

30. Ndi ana a Nadabu: Seledi ndi Apaimu; koma Seledi anamwalira wopanda ana.

31. Ndi mwana wa Apaimu: lsi. Ndi mwana wa lsi: Sesani. Ndi mwana wa Sesani: Alai.

32. Ndi ana a Yada mbale wa Samai: Yeteri, ndi Yonatani; namwalira: Yeteri wopanda ana.

1 Mbiri 2