1 Mafumu 6:36-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ndipo bwalo la m'kati analimanga mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza.

37. Maziko ace a nyumba ya Mulungu anaikidwa m'caka cacinai m'mwezi wa Zivi.

38. Ndipo m'caka cakhumi ndi cimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wacisanu ndi citatu anatsiriza nyumba konse konse monga mwa mamangidwe ace onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.

1 Mafumu 6