26. Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvera mau a Yehova; cifukwa cace Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo.
27. Iye nanena ndi ana ace, nati, Ndimangireni mbereko pa buru. Namangira mbereko.
28. Namuka iye, napeza mtembo wace wogwera m'njira, ndi buru ndi mkango ziti ciimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula buru.
29. Ndipo mneneri ananvamula mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nausenza pa buru, nabwera nao, nalowa m'mudzi mneneri wokalamba kumlira ndi kumuika.