1 Mafumu 1:16-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndipo Batiseba anawerama nalambira mfumu, ndi mfumu niti, Ufunanji?

17. Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomo mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wacifumu.

18. Ndipo tsopano taonani, Adoniva walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu simudziwa.

1 Mafumu 1